
letra de potopa - sagonjah & tadala
[verse 1: sagonjah]
anatiphela, sanativule
anatidyela masuku mitengo sanadule
k-maona ngati apha lathu tsogolo
kuchotsa moyo koma osati ufulu wamalowo
siinathebe ya matafale nkhondo
ndipo sungauthawe wachigamulo moto
akuti amakhiya ukakuwa
koma palibe chisinsi pansi pa dzuwa
ndiulula
kubwera ndiyonamiza lero
sungabwelenso ndiyomweyo pamawa
tamva mabodza mpakana k-mathero
sangatiphonye ife nkhope zambava
lonjezo ndingongole mupeleke
ife kugwira tukwanitsa zaulere
munayamba bwino lero agalatiya
pakadafunda mapeto galu ndikujiwa
[chorus]
pena umangofika potopa
onena ati ati siusimba tsoka
ndalema ndikupirira
mwina vuto ndikusilira
pena umangofika potopa
tizingokhala okoka nkhoka
ndatopa ndikupirira
umphawi sukuzimira
[verse 2: tadala]
pena umangofika potopa polef-ka
chati mbee sichinapse nchowezuka
chilungamo nzidutswa zobenthuka
maumbanda ndi mbiya zosef-ka
nkhani zamaulosi
zonse ndi nthawi la 40 lizakwana
tizanyekesa jabulosi
tizadya katatu patsiku
mmawa, masana, usiku
mawu a saulos
wagalu wakuda samulonjeza chakudya
chachikhumi saiwala wakuba
ndanyozedwa pongokhala wakuda
tikaphana chuma adzatenga ndi atsamunda
ona lero manyasa ndionyasidwa
ofuna chithandizo ndiomanidwa
ozasakidwa ndi mwala okanidwa
ophangira dzulo lero ndiotsamidwa
[chorus]
[outro]
pena umangofika potopa
onena ati siusimba tsoka
ndalema ndikupirira umphawi sukuzimira
ndalema ndikupirira umphawi sukuzimira
letras aleatórias
- letra de what hurts the most (2-4 grooves remix) - cascada
- letra de cry - jamestown story
- letra de figure it out - tk (tania)
- letra de best rapper alive - mart85
- letra de easy/lucky/free - (radio edit) - bright eyes
- letra de drop it like its hot (von tae' remix) - von tae'
- letra de buddy's blues - claudio botelho
- letra de ventre du dragon - filigrann
- letra de after the rain - spa & spa
- letra de she choose me - matthew solo